11 Mʼchaka cha 600 cha moyo wa Nowa, mʼmwezi wachiwiri, pa tsiku la 17 la mweziwo, pa tsiku limeneli madzi onse akumwamba anaphulika ndipo zitseko zotchingira madzi akumwamba zinatseguka.+ 12 Ndiyeno chimvula chinakhuthuka padziko lapansi kwa masiku 40 masana ndi usiku.