42 Mulungu wa bambo anga,+ Mulungu wa Abulahamu amenenso Isaki ankamuopa,+ akanapanda kukhala kumbali yanga, bwenzi mutandibweza kwathu chimanjamanja. Koma Mulungu waona kusautsika kwanga ndi ntchito zimene ndagwira molimbika, nʼchifukwa chake anakudzudzulani usiku wapitawu.”+