-
Ekisodo 18:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Ndiyeno Yetero anati: “Yehova atamandike, amene anakupulumutsani ku Iguputo ndiponso kwa Farao, amenenso analanditsa anthuwa kwa Aiguputo omwe ankawazunza. 11 Tsopano ndadziwa kuti Yehova ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse,+ chifukwa cha zimene anachitira anthu amene ankachita zinthu modzikuza pamaso pa anthu ake.”
-
-
Yoswa 2:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Ndipo anawauza kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani dzikoli+ ndipo tonse tikuchita nanu mantha.+ Aliyense mʼdzikoli mtima wake suli mʼmalo chifukwa cha inu.+ 10 Tinamva mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamene munkachoka ku Iguputo.+ Komanso mmene munaphera mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya* kwa mtsinje wa Yorodano.
-