Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 14:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma chofunika nʼchakuti musapandukire Yehova, ndipo anthu amʼdzikolo musawaope,+ chifukwa ali ngati chakudya kwa ife. Alibenso chitetezo, koma ifeyo Yehova ali nafe.+ Musawaope.”

  • Deuteronomo 20:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iye aziwauza kuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu. Mwatsala pangʼono kumenyana ndi adani anu. Mitima yanu isachite mantha. Musaope, kuchita mantha kapena kunjenjemera chifukwa cha iwo,

  • 2 Mbiri 20:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Choncho Yahazieli anati: “Tamverani Ayuda nonsenu, anthu a ku Yerusalemu ndi inu Mfumu Yehosafati! Yehova akukuuzani kuti, ‘Musaope kapena kuchita mantha ndi gulu lalikululi chifukwa nkhondoyi si yanu, ndi ya Mulungu.+

  • 2 Mbiri 20:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo. Aliyense angoima pamalo ake+ nʼkuona mmene Yehova angakupulumutsireni.+ Inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu, musaope kapena kuchita mantha.+ Mawa mupite kukakumana nawo ndipo Yehova akhala nanu.’”+

  • Salimo 27:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Yehova ndi kuwala kwanga+ komanso ndi amene amandipulumutsa.

      Ndingaope ndani?+

      Yehova ali ngati malo amene amateteza moyo wanga.+

      Ndingachite mantha ndi ndani?

  • Salimo 46:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 46 Mulungu ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu,+

      Thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.+

  • Yesaya 41:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Usachite mantha, chifukwa ndili ndi iwe.+

      Usade nkhawa chifukwa ine ndine Mulungu wako.+

      Ndikulimbitsa, ndithu ndikuthandiza,+

      Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.’

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena