Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 18:25, 26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Mose anasankha amuna oyenerera mu Isiraeli monse kuti akhale atsogoleri a anthu. Anasankha atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10. 26 Choncho iwo ankaweruza anthuwo pakakhala mlandu. Mlandu wovuta ankapita nawo kwa Mose,+ koma mlandu uliwonse waungʼono ankauweruza.

  • Numeri 27:1-5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Kenako ana aakazi a Tselofekadi+ anafika kwa Mose. Tselofekadi anali mwana wa Heferi, Heferi anali mwana wa Giliyadi, Giliyadi anali mwana wa Makiri ndipo Makiri anali mwana wa Manase. Onsewa anali ochokera kumabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana aakazi a Tselofekadi amenewa mayina awo anali Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. 2 Iwo anakaimirira pamaso pa Mose, wansembe Eleazara, atsogoleri+ komanso gulu lonse, pakhomo la chihema chokumanako nʼkunena kuti: 3 “Bambo athu anafera mʼchipululu. Koma iwo sanali mʼgulu la anthu amene ankatsatira Kora,+ omwe anasonkhana kuti atsutsane ndi Yehova. Bambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo, ndipo analibe mwana aliyense wamwamuna. 4 Kodi dzina la bambo athu lisapezekenso ku banja lawo chifukwa chakuti analibe mwana wamwamuna? Chonde, tipatseni cholowa pakati pa azichimwene a bambo athu.” 5 Choncho Mose anapereka dandaulo lawolo pamaso pa Yehova.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena