-
Numeri 14:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Koma Mose anayankha Yehova kuti: “Mukatero, Aiguputo amene anthuwa munawalanditsa mʼmanja mwawo pogwiritsa ntchito mphamvu zanu, adzamva zimenezi.+ 14 Iwo akamva adzauza anthu amʼdziko lino, amenenso amva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu anu,+ komanso kuti mumaonekera kwa iwo pamasomʼpamaso.+ Inu ndinu Yehova, ndipo mtambo wanu uli pamwamba pawo. Masana mumawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha mtambo, pamene usiku mumawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha moto.+
-