Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 22:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Chifukwa chofunda chake nʼchomwecho. Ndi nsalu imene amafunda.+ Nanga afunda chiyani pogona? Ndiyeno akandilirira, ine ndidzamva ndithu, chifukwa ndine wachifundo.+

  • 2 Mbiri 30:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Mukabwerera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo ndi anthu amene anawagwira+ ndipo adzawalola kubwerera mʼdzikoli.+ Chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi wachisomo komanso wachifundo+ ndipo sadzayangʼana kumbali mukabwerera kwa iye.”+

  • Nehemiya 9:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire zinthu zodabwitsa zimene munawachitira. Mʼmalomwake anaumitsa khosi ndipo anasankha munthu woti awatsogolere pobwereranso ku ukapolo ku Iguputo.+ Koma inu ndinu Mulungu wokonzeka kukhululuka, wachisomo, wachifundo, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika*+ chochuluka, choncho simunawasiye.+

  • Salimo 86:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima,

      Wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka ndiponso wokhulupirika.*+

  • Yoweli 2:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ngʼambani mitima yanu,+ osati zovala zanu,+

      Ndipo bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,

      Chifukwa iye ndi wachifundo, wokoma mtima, wosakwiya msanga+ ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka.+

      Iye adzasintha maganizo okubweretserani tsoka.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena