-
Nehemiya 9:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire zinthu zodabwitsa zimene munawachitira. Mʼmalomwake anaumitsa khosi ndipo anasankha munthu woti awatsogolere pobwereranso ku ukapolo ku Iguputo.+ Koma inu ndinu Mulungu wokonzeka kukhululuka, wachisomo, wachifundo, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika*+ chochuluka, choncho simunawasiye.+
-
-
Yona 4:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Choncho iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Inu Yehova, kodi zimene ndimaopa ndili kwathu zija si zimenezi? Nʼchifukwa chaketu ndinkafuna kuthawira ku Tarisi.+ Ndinadziwa kuti inu ndinu Mulungu wachifundo, wokoma mtima, wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka+ komanso mumamva chisoni mukafuna kubweretsa tsoka.
-