Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Mukamaweruza mlandu wa munthu wosauka musamamukondere chifukwa choti ndi wosauka.+

  • Deuteronomo 1:16, 17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Pa nthawi imeneyo ndinauza oweruza anu kuti, ‘Mukamaweruza mlandu pakati pa abale anu, muziweruza mwachilungamo+ pakati pa munthu ndi mʼbale wake kapena ndi mlendo.+ 17 Musamakondere poweruza mlandu.+ Munthu wamba ndi munthu wolemekezeka, onse muziwamvetsera chimodzimodzi.+ Musamaope anthu+ chifukwa mukuweruzira Mulungu+ ndipo ngati mlandu wakuvutani muzibwera nawo kwa ine kuti ndiumve.’+

  • Deuteronomo 16:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Musamakhotetse chilungamo,+ musamakondere+ kapena kulandira chiphuphu, chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru+ komanso kupotoza mawu a anthu olungama.

  • 2 Mbiri 19:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndiyeno anauza oweruzawo kuti: “Muzichita zinthu mosamala chifukwa simukuweruzira munthu koma Yehova, ndipo iye ali nanu pa ntchito yoweruzayi.+

  • Aroma 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Chifukwa Mulungu alibe tsankho.+

  • Yakobo 2:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma mukapitiriza kukhala okondera,+ mukuchita tchimo ndipo lamulo likusonyezeratu* kuti ndinu olakwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena