-
Deuteronomo 26:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 “Mukakalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu, ndipo mukakalitengadi nʼkumakhalamo, 2 mukatenge zina mwa zipatso zoyambirira pa zokolola* zonse zamʼmunda mwanu zimene mudzakolole mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Mukaziike mʼdengu nʼkupita nazo kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuika dzina lake.+
-