-
Deuteronomo 18:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Pakati panu pasapezeke munthu wowotcha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ aliyense wochita zamatsenga,+ aliyense woombeza,+ wanyanga,+ 11 aliyense wochesula* ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu+ kapena wolosera zamʼtsogolo,+ kapena aliyense wofunsira kwa akufa.+ 12 Chifukwa aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akuchita zimenezi, Yehova Mulungu wanu akuwathamangitsa pamaso panu.
-
-
Yesaya 8:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Ndipo atakuuzani kuti: “Funsirani kwa anthu olankhula ndi mizimu kapena anthu olosera zamʼtsogolo, omwe amalira ngati mbalame ndiponso kulankhula motsitsa mawu,” kodi mungavomere? Kodi mtundu uliwonse wa anthu suyenera kufunsira kwa Mulungu wake? Kodi akuyenera kufunsira kwa anthu akufa pofuna kuthandiza anthu amoyo?+
-