Ekisodo 18:15, 16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Mose anayankha apongozi akewo kuti: “Chifukwa anthuwa akumabwera kwa ine kuti adzamve malangizo a Mulungu. 16 Akakhala ndi mlandu pakati pawo akumabwera nawo kwa ine, ndipo ndikumaweruza nʼkuwauza chigamulo cha Mulungu woona ndi malamulo ake.”+ Numeri 15:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Aisiraeli ali mʼchipululumo, tsiku lina anapeza munthu wina akutola nkhuni pa tsiku la Sabata.+ Numeri 15:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Iwo anamutsekera+ chifukwa panalibe lamulo lachindunji la zimene ayenera kuchita ndi munthuyo.
15 Mose anayankha apongozi akewo kuti: “Chifukwa anthuwa akumabwera kwa ine kuti adzamve malangizo a Mulungu. 16 Akakhala ndi mlandu pakati pawo akumabwera nawo kwa ine, ndipo ndikumaweruza nʼkuwauza chigamulo cha Mulungu woona ndi malamulo ake.”+