-
Yesaya 61:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
61 Mzimu wa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, uli pa ine,+
Chifukwa Yehova anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.+
Anandituma kuti ndikamange mabala a anthu osweka mtima,
Kuti ndilengeze za ufulu kwa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,
Komanso kuti maso a akaidi adzatsegulidwa.+
2 Wandituma kuti ndilengeze za chaka cha Yehova chokomera anthu mtima,*
Ndi za tsiku lobwezera la Mulungu wathu,+
Komanso kuti nditonthoze anthu onse amene akulira,+
-
Luka 4:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 “Mzimu wa Yehova* uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu osauka. Anandituma kudzalengeza za ufulu kwa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina komanso zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale pa ufulu,+ 19 ndi kudzalalikira za chaka chovomerezeka kwa Yehova.”*+
-
-
-