-
Levitiko 19:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Mwamuna akagona ndi kapolo wamkazi amene mbuye wake anamulonjeza kuti adzamupereka kwa mwamuna wina, koma mkaziyo sanawomboledwe kapena kupatsidwa ufulu, pazikhala chilango. Koma iwo asaphedwe chifukwa mkaziyo anali asanakhale mfulu. 21 Mwamunayo azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo ya nsembe yakupalamula pakhomo la chihema chokumanako.+
-
-
Numeri 6:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Munthuyo aziyambiranso masiku ake odzipereka kwa Yehova ngati Mnaziri, ndipo azibweretsa nkhosa yaingʼono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi monga nsembe yakupalamula. Koma masiku oyamba aja sadzawerengedwa chifukwa anadetsa unaziri wake.
-