Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 23:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Mukalonjeza kanthu kwa Yehova Mulungu wanu+ musamachedwe kukwaniritsa zimene mwalonjezazo.+ Chifukwa Yehova Mulungu wanu adzafuna ndithu kuti mukwaniritse zimene mwalonjezazo. Mukapanda kutero mudzakhala kuti mwachimwa.+

  • Salimo 116:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,

      Pamaso pa anthu ake onse.+

  • Salimo 119:106
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 106 Ndalumbira kuti ndidzasunga zigamulo zanu zolungama,

      Ndipo ndidzakwaniritsa lumbiro langa.

  • Mlaliki 5:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako,+ chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu opusa.+ Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.+

  • Mateyu 5:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Musamalumbire koma osachita,+ mʼmalomwake muzikwaniritsa zimene mwalonjeza kwa Yehova.’*+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena