14 Ngakhale zili choncho, ndakupeza ndi milandu ingapo. Iwe kumeneko uli ndi anthu amene akupitiriza kutsatira chiphunzitso cha Balamu,+ amene anaphunzitsa Balaki+ kuti aikire ana a Isiraeli chopunthwitsa kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi kuchita chiwerewere.+