-
Yoswa 20:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya mʼdera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ mʼdera lamapiri la Efuraimu komanso Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, mʼdera lamapiri la Yuda. 8 Kuchigawo cha Yorodano, kumʼmawa kwa Yeriko, anasankha Bezeri,+ mʼchipululu cha mʼdera lokwererapo la fuko la Rubeni. Anasankhanso Ramoti+ ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi komanso Golani+ ku Basana mʼdera la fuko la Manase.+
-