-
Ekisodo 29:27, 28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Pankhosa yoikira Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe, upatule chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku, ndi mwendo wa gawo lopatulika umene anapereka.+ 28 Zimenezi zikhale za Aroni ndi ana ake mwa lamulo mpaka kalekale. Aisiraeli ayenera kutsatira lamulo limeneli chifukwa ndi gawo lopatulika. Lidzakhala gawo lopatulika loyenera kuperekedwa ndi Aisiraeli.+ Limeneli ndi gawo lawo lopatulika loperekedwa kwa Yehova kuchokera pansembe zawo zamgwirizano.+
-
-
Deuteronomo 18:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Tsopano zinthu zimene ansembe azidzalandira kuchokera kwa anthu ndi izi: Amene akupereka nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa, azipereka kwa wansembe mwendo wakutsogolo, nsagwada ndi chifu.
-