17 Mulungu anamva pemphero la Leya ndipo anakhala woyembekezera. Patapita nthawi, Leya anaberekera Yakobo mwana wamwamuna wa 5. 18 Mwanayo atabadwa, Leya anati: “Mulungu wandipatsa mphoto chifukwa ndapereka kapolo wanga kwa mwamuna wanga.” Choncho Leya anapatsa mwanayo dzina lakuti Isakara.+