Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 4:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Pamene mukusamutsa msasa, Aroni ndi ana ake azikhala atamaliza kuphimba zinthu za mʼmalo oyera+ ndi ziwiya zonse za mʼmalo oyerawo. Kenako ana a Kohati azibwera nʼkudzazinyamula+ koma iwo asamakhudze zinthu za mʼmalo oyerazo chifukwa akatero adzafa.+ Ana a Kohati ndi amene ali ndi udindo wonyamula zinthu zimenezi pachihema chokumanako.

  • Numeri 4:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Ana a Kohatiwo asadzalowe kuti akaone zinthu zopatulikazo ngakhale pangʼono pokha chifukwa akadzatero adzafa.”+

  • Numeri 16:39, 40
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Choncho wansembe Eleazara anatenga zofukizira zakopa zimene anthu amene anapsa ndi moto aja anabweretsa, ndipo anazisula nʼkupanga timalata tokutira guwa lansembe, 40 mogwirizana ndi zimene Yehova anamuuza kudzera mwa Mose. Timalatato tinali chikumbutso kwa Aisiraeli kuti munthu wamba* amene si mbadwa ya Aroni asayandikire kwa Yehova kuti akapereke nsembe zofukiza.+ Anachita zimenezi kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi anthu amene ankamutsatira anachita.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena