-
Numeri 23:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Balaki anauza Balamu kuti: “Tiyeni tipite kumalo ena kumene mungathe kuwaona anthuwo. Simukaona onse, koma mukangoona ochepa. Mukatemberere amenewo.”+ 14 Choncho anamutengera ku Zofimu, pamwamba pa phiri la Pisiga.+ Kumeneko anamanga maguwa ansembe 7, nʼkupereka nsembe ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+
-
-
Numeri 23:28-30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Choncho Balaki anatenga Balamu nʼkupita naye pamwamba pa phiri la Peori, limene linayangʼanizana ndi Yesimoni.*+ 29 Kenako Balamu anauza Balaki kuti: “Mumange maguwa ansembe 7 pamalo ano ndipo mundikonzere ngʼombe zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7.”+ 30 Choncho Balaki anachita zimene Balamu ananena ndipo anapereka nsembe ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.
-