7 Amunawo anakamenyana ndi Amidiyani, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose, ndipo anapha mwamuna aliyense. 8 Anthu amene anaphedwawo akuphatikizapo mafumu 5 a Chimidiyani. Mafumuwo anali Evi, Rekemu, Zuri, Hura ndi Reba. Komanso anapha Balamu+ mwana wa Beori ndi lupanga.