-
Deuteronomo 7:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 “Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani mʼdziko limene mwatsala pangʼono kulitenga kuti likhale lanu,+ adzakuchotseraninso mitundu ikuluikulu.+ Adzakuchotserani Ahiti, Agirigasi, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ mitundu 7 ikuluikulu komanso yamphamvu kuposa inu.+ 2 Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu ndipo mudzawagonjetsa.+ Mudzawawononge+ ndithu ndipo musadzachite nawo pangano lililonse kapena kuwakomera mtima.+
-