Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 1:2, 3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse apadziko lapansi.+ Iye wandituma kuti ndimumangire nyumba ku Yerusalemu+ mʼdziko la Yuda. 3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye ndipo apite ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda nʼkukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli. Iye ndi Mulungu woona ndipo nyumba yake inali ku Yerusalemu.*

  • Salimo 147:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Yehova akumanga Yerusalemu.+

      Akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli amene anapita ku ukapolo.+

  • Yeremiya 32:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 ‘Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumayiko onse kumene ndinawabalalitsira nditakwiya, kupsa mtima ndiponso ndili ndi ukali waukulu.+ Ndidzawabwezeretsa mʼdziko lino nʼkuwachititsa kuti azikhala motetezeka.+

  • Ezekieli 34:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Nkhosa zanga ndidzazitulutsa pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzazisonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmayiko ena nʼkuzibweretsa mʼdziko lawo. Ndidzazidyetsa mʼmapiri a ku Isiraeli,+ mʼmphepete mwa mitsinje komanso pafupi ndi malo onse amʼdzikolo kumene kumakhala anthu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena