Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 20:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Musaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wanu, ndine Mulungu amene ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,+ amene ndimalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.

  • Ekisodo 34:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Musagwadire mulungu wina,+ chifukwa Yehova amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.* Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.*+

  • Numeri 25:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, wabweza mkwiyo wanga pa Aisiraeli, chifukwa sanalekerere ngakhale pangʼono kuti anthu azipikisana nane pakati pawo.+ Choncho sindinawononge Aisiraeliwa, ngakhale kuti ndimafuna kuti anthu azikhala odzipereka kwa ine ndekha.+

  • Mateyu 4:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Choka Satana! Chifukwa Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira+ ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena