-
Levitiko 24:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Pagulu lililonse la mikateyo uike lubani weniweni. Lubaniyo aziperekedwa nsembe yowotcha pamoto+ kwa Yehova kuimira nsembe yonseyo. 8 Pa tsiku lililonse la Sabata azikhazika mkatewo pamaso pa Yehova nthawi zonse.+ Limeneli ndi pangano pakati pa ine ndi Aisiraeli mpaka kalekale. 9 Mkatewo uzikhala wa Aroni ndi ana ake,+ ndipo aziudyera mʼmalo oyera,+ chifukwa waperekedwa kwa iye monga chinthu choyera koposa kuchokera pa nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova. Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale.”
-
-
Maliko 2:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita, iyeyo ndi amuna omwe anali naye atamva njala ndipo analibiretu chilichonse?+ 26 Nkhani yonena za Abiyatara+ wansembe wamkulu imanena kuti, Davide analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo anadya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,* umene aliyense sankayenera kudya malinga ndi malamulo koma ansembe okha.+ Iye anatenga mitanda ina ya mkatewo nʼkupatsa amuna amene anali naye limodzi. Kodi inu simunawerenge nkhani imeneyi?”
-
-
Luka 6:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Koma Yesu anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita, iyeyo ndi amuna omwe anali naye atamva njala?+ 4 Kodi simunawerenge kuti analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo anadya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,* imene iye ndi anthu omwe anali nawo aja sankayenera kudya malinga ndi malamulo, koma ansembe okha?”+
-