36 Kenako mfumu inaitanitsa Simeyi+ nʼkumuuza kuti: “Umange nyumba yako ku Yerusalemu ndipo uzikhala kumeneko. Usadzachokeko nʼkupita kwina kulikonse. 37 Tsiku limene udzachoke nʼkudutsa chigwa cha Kidironi,+ udziwiretu kuti udzafa. Mlandu wa magazi ako udzakhala pamutu pako.”