Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 4:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Pamene mukusamutsa msasa, Aroni ndi ana ake azikhala atamaliza kuphimba zinthu za mʼmalo oyera+ ndi ziwiya zonse za mʼmalo oyerawo. Kenako ana a Kohati azibwera nʼkudzazinyamula+ koma iwo asamakhudze zinthu za mʼmalo oyerazo chifukwa akatero adzafa.+ Ana a Kohati ndi amene ali ndi udindo wonyamula zinthu zimenezi pachihema chokumanako.

  • Numeri 7:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma ana a Kohati sanawapatse zinthu zimenezi, chifukwa ntchito yawo inali yokhudza utumiki wapamalo oyera.+ Iwo ankanyamula zinthu zopatulika pamapewa awo.+

  • 1 Mbiri 15:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pa nthawi imeneyi mʼpamene Davide ananena kuti: “Alevi okha ndi amene ayenera kunyamula Likasa la Mulungu woona, chifukwa Yehova anasankha iwowa kuti azinyamula Likasa la Yehova ndiponso azimutumikira nthawi zonse.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena