-
2 Mbiri 24:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Ngakhale kuti asilikali a Siriya amene anabwera anali ochepa, Yehova anapereka mʼmanja mwawo gulu lalikulu kwambiri la asilikali+ chifukwa iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo. Choncho Asiriyawo anapereka chiweruzo kwa Yehoasi. 25 Asilikaliwo atachoka (nʼkumusiya atavulala kwambiri), atumiki ake anamʼkonzera chiwembu chifukwa anapha ana* a wansembe Yehoyada.+ Iwo anamuphera pabedi lake.+ Kenako anamuika mʼmanda mu Mzinda wa Davide+ koma sanamuike mʼmanda a mafumu.+
-