23 Mʼchaka cha 7, Yehoyada anachita zinthu molimba mtima ndipo anachita pangano ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100.+ Atsogoleriwo anali Azariya mwana wa Yerohamu, Isimaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri.