Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 25:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 ‘Ndiyeno zaka 70 zimenezo zikadzakwana,+ ndidzalanga mfumu ya Babulo ndi mtundu umenewo chifukwa cha zolakwa zawo.+ Ndipo dziko la Akasidi ndidzalisandutsa bwinja mpaka kalekale,’ akutero Yehova.+

  • Yeremiya 29:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndidzakulolani kuti mundipeze,’+ akutero Yehova. ‘Ndidzasonkhanitsa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kumayiko ena kuchokera mʼmitundu yonse ndi kumalo onse kumene ndinakubalalitsirani,’+ akutero Yehova. ‘Kenako ndidzakubwezeretsani kumalo amene ndinakuchotsani pa nthawi imene ndinakupititsani ku ukapolo.’+

  • Yeremiya 33:10, 11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Yehova wanena kuti: ‘Pamalo ano amene mudzanene kuti ndi bwinja, opanda anthu kapena ziweto, mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu imene yawonongeka, moti mulibe anthu ndipo simukukhala aliyense ngakhale ziweto, mʼmalo amenewa mudzamveka 11 phokoso la chikondwerero ndi chisangalalo.+ Mudzamvekanso mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi komanso mawu a anthu amene akunena kuti: “Yamikani Yehova wa magulu ankhondo akumwamba chifukwa Yehova ndi wabwino+ ndipo chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale!”’+

      ‘Anthuwo adzabweretsa nsembe zoyamikira kunyumba ya Yehova,+ chifukwa ndidzabwezeretsa anthu amʼdzikoli, amene anatengedwa kupita kudziko lina, kuti akhalenso ngati mmene analili poyamba,’ akutero Yehova.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena