-
Numeri 18:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni kuti: “Ine ndakupatsa udindo woyangʼanira zinthu zonse zimene anthu azipereka kwa ine.+ Pa zinthu zonse zopatulika zimene Aisiraeli azipereka, ndakupatsa gawo iweyo ndi ana ako, kuti likhale lanu mpaka kalekale.+ 9 Gawo limene muzilandira lizichokera pa nsembe zonse zopatulika koposa zowotcha pamoto. Nsembe zake ndi izi: nsembe zilizonse zimene angapereke kwa ine, kuphatikizapo nsembe zawo zambewu,+ nsembe zawo zamachimo+ komanso nsembe zawo zakupalamula.+ Gawolo lizikhala chinthu chopatulika koposa kwa iwe ndi ana ako.
-