-
Deuteronomo 15:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse muzimasula anthu amene anakongola zinthu zanu.+ 2 Muzichita izi pomasula anthu angongolewo: Munthu aliyense azimasula mnzake amene ali ndi ngongole yake. Asamakakamize mnzake kapena mʼbale wake kuti abweze ngongoleyo, chifukwa chilengezo choti anthu angongole amasuke chaperekedwa potsatira lamulo la Yehova.+ 3 Mlendo mungathe kumukakamiza kuti abweze ngongole,+ koma ngati mʼbale wanu wakongola chinthu chanu chilichonse, musamukakamize kuti achibweze.
-