-
Numeri 14:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Aisiraeli onse anayamba kungʼungʼudzira Mose ndi Aroni,+ ndipo gulu lonselo linati: “Zikanakhala bwino tikanangofera ku Iguputo, kapena tikanangofera mʼchipululu muno. 3 Nʼchifukwa chiyani Yehova watibweretsa kudziko lino kuti tidzaphedwe ndi lupanga?+ Akazi athu ndi ana athu adzatengedwa ndi adani.+ Kodi si bwino kuti tingobwerera ku Iguputo?”+ 4 Iwo anafika ngakhale pouzana kuti: “Tiyeni tisankhe mtsogoleri, tibwerere ku Iguputo!”+
-