Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yoswa 7:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Akanani ndi anthu onse a mʼdzikoli adzamva zimenezi, ndipo adzabwera nʼkufafaniza dzina lathu padziko lapansi. Ndiye mudzateteza bwanji dzina lanu lalikulu?”+

  • 1 Samueli 12:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Chifukwa cha dzina lake lalikulu,+ Yehova sadzasiya anthu ake,+ popeza Yehova wafuna kuti inuyo mukhale anthu ake.+

  • 2 Mbiri 14:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndiyeno Asa anayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu wake+ kuti: “Inu Yehova, zilibe kanthu kuti anthu amene mukufuna kuwathandizawo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu.+ Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu,+ ndipo tabwera mʼdzina lanu kudzamenyana ndi chigulu cha anthuchi.+ Inu Yehova ndinu Mulungu wathu. Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.”+

  • Salimo 115:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 115 Ife sitikuyenera, inu Yehova, ife sitikuyenera,

      Koma ulemerero ukuyenera kupita ku dzina lanu+

      Chifukwa cha kukhulupirika kwanu komanso chikondi chanu chokhulupirika.+

       2 Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti:

      “Mulungu wawo ali kuti?”+

  • Yesaya 48:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Koma ndidzabweza mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa.+

      Chifukwa cha ulemerero wanga, ine ndidzadziletsa

      Ndipo sindidzakuwonongani.+

  • Yeremiya 14:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Ngakhale kuti machimo athu akuchitira umboni kuti ndife olakwa,

      Inu Yehova, chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu.+

      Chifukwa zochita zathu zosonyeza kusakhulupirika nʼzambiri,+

      Ndipo takuchimwirani.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena