-
Yoswa 9:18-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Koma Aisiraeli sanawaphe anthuwo chifukwa atsogoleri awo anali atalumbirira anthuwo mʼdzina la Yehova,+ Mulungu wa Isiraeli. Choncho gulu lonse linayamba kungʼungʼudza motsutsana ndi atsogoleriwo. 19 Ndiyeno atsogoleri onse anauza gululo kuti: “Ife tinawalumbirira mʼdzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli, ndiye sitingawaphe. 20 Tipanga chonchi: Tiwasiya kuti akhale ndi moyo, kuti Mulungu asatikwiyire popeza tinawalumbirira.”+
-
-
Oweruza 11:34, 35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Kenako Yefita anabwerera kwawo ku Mizipa+ ndipo akufika anangoona mwana wake wamkazi akubwera kudzamʼchingamira, akuimba maseche komanso akuvina. Iye anali mwana yekhayo amene anali naye. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. 35 Atangomuona, anangʼamba zovala zake nʼkunena kuti: “Mayine mwana wanga! Ndikumva chisoni kwambiri chifukwa ndikukuchotsa pakhomo. Ndalonjeza kwa Yehova ndipo sindingathe kubweza mawu anga.”+
-
-
Salimo 50:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Yamikani Mulungu kuti ikhale ngati nsembe imene mukupereka kwa iye,+
Ndipo perekani kwa Wamʼmwambamwamba zimene mwalonjeza.+
-