Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 2:8, 9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Tandipempha, ndipo ndikupatsa mitundu ya anthu kuti ikhale cholowa chako,

      Ndiponso dziko lonse lapansi kuti likhale lako.+

       9 Mitunduyo udzaiphwanya ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+

      Ndipo udzaiswa ngati chiwiya chadothi.”+

  • Salimo 45:4, 5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Upite mu ulemerero wako ndipo upambane.*+

      Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo,+

      Ndipo dzanja lako lamanja lidzachita* zinthu zochititsa mantha.

       5 Mivi yako ndi yakuthwa ndipo ikuchititsa kuti anthu agwe pamaso pako.+

      Imalasa mitima ya adani a mfumu.+

  • Mateyu 28:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Tsopano Yesu anayandikira nʼkuwauza kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.+

  • Chivumbulutso 6:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Nditayangʼana, ndinaona hatchi yoyera+ ndipo amene anakwera pahatchiyi ananyamula uta. Iye anapatsidwa chisoti chachifumu+ nʼkupita kukagonjetsa adani ake ndipo anapambana pankhondo yolimbana nawo.+

  • Chivumbulutso 12:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mkaziyo anabereka mwana wamwamuna,+ mnyamata amene adzakusa mitundu yonse ya anthu ndi ndodo yachitsulo.+ Ndipo mwana wakeyo anatengedwa msangamsanga nʼkupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu.

  • Chivumbulutso 19:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera.+ Amene anakwera pahatchiyo dzina lake linali lakuti Wokhulupirika+ ndi Woona.+ Iye amaweruza molungama ndipo akumenya nkhondo mwachilungamo.+

  • Chivumbulutso 19:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Mʼkamwa mwake munkatuluka lupanga lalitali+ lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo.+ Komanso iye ankapondaponda muchopondera mphesa cha mkwiyo waukulu wa Mulungu Wamphamvuyonse.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena