Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 28:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:

      “Ndikuika mwala woyesedwa mu Ziyoni kuti ukhale maziko,+

      Umenewu ndi mwala wapakona wamtengo wapatali+ wa maziko olimba.+

      Palibe munthu woukhulupirira amene adzade nkhawa.+

  • Luka 20:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Koma iye anawayangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Paja malemba amanena kuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana, wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.’*+ Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani?

  • Machitidwe 4:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yesu ameneyu ndi ‘mwala umene inu omanga nyumba munauona ngati wopanda pake, umene tsopano wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.’+

  • 1 Akorinto 3:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Chifukwa palibe munthu wina amene angayale maziko ena kupatulapo amene anayalidwa kale, omwe ndi Yesu Khristu.+

  • Aefeso 2:19, 20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Choncho, si inunso anthu osadziwika kapena alendo,+ koma mofanana ndi oyerawo inunso ndinu nzika+ ndipo ndinu a mʼbanja la Mulungu.+ 20 Mwamangidwa pamaziko a atumwi ndi aneneri+ ndipo Khristu Yesu ndi mwala wapakona wa mazikowo.+

  • 1 Petulo 2:4-7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pamene mukubwera kwa Ambuye, amene ndi mwala wamoyo umene anthu anaukana,+ koma umene Mulungu anausankha, umenenso ndi wamtengo wapatali kwa Mulunguyo,+ 5 inunso monga miyala yamoyo mukumangidwa nʼkukhala nyumba yauzimu+ kuti mudzakhale ansembe oyera. Monga ansembe oyera muzidzapereka nsembe zauzimu+ zovomerezeka pamaso pa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.+ 6 Paja Lemba limati: “Inetu ndikuika mwala wosankhidwa mwapadera mu Ziyoni. Umenewu ndi mwala wapakona ya maziko, womwe ndi wamtengo wapatali, ndipo aliyense wokhulupirira mwalawo sadzakhumudwa.”*+

      7 Choncho iye ndi wamtengo wapatali kwa inu chifukwa mumamukhulupirira. Koma kwa amene samukhulupirira, “mwala umene omanga nyumba anaukana,+ wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena