13 Wosangalala ndi munthu amene amapeza nzeru,+
Ndiponso munthu amene amaphunzira zinthu zimene zingamuthandize kukhala wozindikira.
14 Chifukwa kupeza nzeru nʼkwabwino kuposa kupeza siliva,
Ndipo kukhala nazo monga phindu nʼkwabwino kuposa kukhala ndi golide.+
15 Nʼzamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,
Palibe chimene umalakalaka chimene chingafanane nazo.