2 Ndiyeno mfumuyo inauza mneneri Natani+ kuti: “Ine ndikukhala mʼnyumba ya mitengo ya mkungudza,+ pamene Likasa la Mulungu woona likukhala mutenti.”+ 3 Natani anauza mfumu kuti: “Chitani chilichonse chimene mtima wanu ukufuna, chifukwa Yehova ali nanu.”+