2 Samueli 12:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ndiyeno Natani anauza Davide kuti: “Munthu ameneyu ndi iweyo. Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndinakudzoza kuti ukhale mfumu ya Isiraeli+ ndipo ndinakupulumutsa mʼmanja mwa Sauli.+ 2 Samueli 12:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Nʼchifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova pochita zoipa pamaso pake? Unapha Uriya Muhiti ndi lupanga.+ Kenako unatenga mkazi wake kuti akhale mkazi wako+ utapha Uriyayo ndi lupanga la Aamoni.+ Miyambo 17:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Kudzudzula kumamufika pamtima munthu womvetsa zinthu,+Kuposa kukwapula munthu wopusa zikwapu 100.+ Agalatiya 6:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Abale, ngati munthu wapatuka nʼkuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu amene ndi oyenerera mwauzimu, yesani kuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Koma pamene mukuchita zimenezi musamale,+ kuopera kuti inunso mungayesedwe.+
7 Ndiyeno Natani anauza Davide kuti: “Munthu ameneyu ndi iweyo. Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndinakudzoza kuti ukhale mfumu ya Isiraeli+ ndipo ndinakupulumutsa mʼmanja mwa Sauli.+
9 Nʼchifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova pochita zoipa pamaso pake? Unapha Uriya Muhiti ndi lupanga.+ Kenako unatenga mkazi wake kuti akhale mkazi wako+ utapha Uriyayo ndi lupanga la Aamoni.+
10 Kudzudzula kumamufika pamtima munthu womvetsa zinthu,+Kuposa kukwapula munthu wopusa zikwapu 100.+
6 Abale, ngati munthu wapatuka nʼkuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu amene ndi oyenerera mwauzimu, yesani kuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Koma pamene mukuchita zimenezi musamale,+ kuopera kuti inunso mungayesedwe.+