Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 8:66
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 66 Tsiku lotsatira,* Solomo anauza anthuwo kuti azipita, ndipo anthuwo anadalitsa mfumuyo nʼkumapita kwawo. Anapita akusangalala, ali ndi chimwemwe mumtima chifukwa cha zabwino zonse+ zimene Yehova anachitira Davide mtumiki wake komanso anthu ake Aisiraeli.

  • Salimo 13:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Ndidzaimbira Yehova chifukwa wandipatsa mphoto yaikulu.+

  • Salimo 31:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ubwino wanu ndi wochuluka kwambiri!+

      Ubwino umenewu mwasungira anthu amene amakuopani,+

      Ndipo mwausonyeza kwa anthu amene amathawira kwa inu, pamaso pa anthu onse.+

  • Yesaya 63:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Ndidzanena za ntchito za Yehova zosonyeza chikondi chake chokhulupirika,

      Ntchito zotamandika za Yehova,

      Chifukwa cha zinthu zonse zimene Yehova watichitira.+

      Zinthu zabwino zambiri zimene wachitira nyumba ya Isiraeli,

      Mogwirizana ndi chifundo chake komanso chikondi chake chokhulupirika chomwe ndi chochuluka.

  • Yeremiya 31:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iwo adzabwera nʼkufuula mosangalala pamwamba pa phiri la Ziyoni.+

      Nkhope zawo zidzawala chifukwa cha ubwino wa* Yehova.

      Chifukwa cha mbewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta,

      Ndiponso chifukwa cha ana a nkhosa ndi ana a ngʼombe.+

      Iwo adzakhala ngati dimba lothiriridwa bwino+

      Ndipo sadzakhalanso ofooka.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena