-
2 Samueli 7:15-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndipo chikondi changa chokhulupirika sichidzachoka pa iye ngati mmene ndinachichotsera pa Sauli,+ amene ndinamʼchotsa pamaso pako. 16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhalapobe mpaka kalekale. Mpando wako wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.”’”+
17 Natani anauza Davide mawu onsewa ndiponso masomphenya onse amene anaona.+
-
-
1 Mafumu 3:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Solomo atamva zimenezi anati: “Inu mwasonyeza kwambiri chikondi chokhulupirika kwa mtumiki wanu Davide bambo anga, chifukwa anali wokhulupirika, wachilungamo komanso wowongoka mtima pamaso panu. Mwapitiriza kumusonyeza chikondi chimenechi mpaka pano pomupatsa mwana kuti akhale pampando wake wachifumu.+
-