2 Samueli 15:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Kenako Davide anauzidwa kuti: “Ahitofeli nayenso ali mʼgulu la anthu amene akukonza chiwembu+ ndi Abisalomu.”+ Davide atamva zimenezi anati: “Chonde Yehova,+ chititsani kuti malangizo a Ahitofeli akhale opusa.”+ 2 Samueli 17:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Ahitofeli ataona kuti malangizo ake sanatsatiridwe, anakwera bulu nʼkupita kunyumba yake mʼtauni yakwawo.+ Kenako anapereka malangizo kwa anthu amʼbanja lake+ ndipo atatero anadzimangirira.+ Iye anafa ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake. Salimo 7:14, 15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Taonani munthu amene ali ndi pakati pa zinthu zoipa,Watenga pakati pa mavuto ndipo adzabereka mabodza.+ 15 Iye wakumba dzenje ndipo walizamitsa,Koma adzagwera mʼdzenje limene wakumba yekhalo.+
31 Kenako Davide anauzidwa kuti: “Ahitofeli nayenso ali mʼgulu la anthu amene akukonza chiwembu+ ndi Abisalomu.”+ Davide atamva zimenezi anati: “Chonde Yehova,+ chititsani kuti malangizo a Ahitofeli akhale opusa.”+
23 Ahitofeli ataona kuti malangizo ake sanatsatiridwe, anakwera bulu nʼkupita kunyumba yake mʼtauni yakwawo.+ Kenako anapereka malangizo kwa anthu amʼbanja lake+ ndipo atatero anadzimangirira.+ Iye anafa ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake.
14 Taonani munthu amene ali ndi pakati pa zinthu zoipa,Watenga pakati pa mavuto ndipo adzabereka mabodza.+ 15 Iye wakumba dzenje ndipo walizamitsa,Koma adzagwera mʼdzenje limene wakumba yekhalo.+