25 Sauli anati: “Mukauze Davide kuti, ‘Sikuti mfumu ikufuna malowolo,+ koma ikungofuna makungu amene amachotsa pochita mdulidwe a Afilisiti okwana 100,+ kuti ibwezere adani ake.’” Koma pamenepa Sauli ankakonza chiwembu kuti Davide aphedwe ndi Afilisiti.