-
1 Samueli 25:32, 33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Zitatero, Davide anauza Abigayeli kuti: “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene wakutumiza kudzakumana ndi ine lero! 33 Iwenso udalitsike chifukwa cha kuganiza bwino kwako. Udalitsike chifukwa chondiletsa kuti ndisapalamule mlandu wa magazi+ ndiponso kuti ndisabwezere* ndekha ndi manja anga.
-