1 Pachiyambi, panali wina amene ankadziwika kuti Mawu,+ ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu+ komanso Mawuyo anali mulungu.+ 2 Ameneyu anali ndi Mulungu kuyambira pachiyambi. 3 Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye+ ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.