-
1 Mafumu 2:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Kenako Mfumu Solomo analumbira pamaso pa Yehova kuti: “Mulungu andilange mowirikiza ngati Adoniya sanaike moyo wake pangozi popempha zimenezi. 24 Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, amene anandiika pampando wachifumu wa Davide bambo anga komanso amene anachititsa kuti ufumu wanga ukhazikike+ ndiponso kuti pakhale mzere wa banja lachifumu+ mogwirizana ndi zimene analonjeza, lero Adoniya aphedwa.”+
-