-
Nehemiya 6:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 nthawi yomweyo Sanibalati ndi Gesemu ananditumizira uthenga wakuti: “Bwera tidzapangane nthawi yoti tikakumane mʼmudzi wina mʼchigwa cha Ono.”+ Koma ankandikonzera chiwembu. 3 Choncho ndinatumiza anthu kuti akawauze kuti: “Ntchito imene ndikugwirayi ndi yaikulu ndipo sindingathe kubwera. Kodi ntchitoyi iime chifukwa chakuti ine ndabwera kumeneko?”
-