-
2 Samueli 15:32-34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Davide atafika pamwamba pa phiri, pomwe anthu ankapita kukalambira Mulungu, anaona Husai+ mbadwa ya Areki+ akubwera kudzakumana naye, atangʼamba mkanjo wake ndiponso atadzithira dothi kumutu. 33 Davide anamuuza kuti: “Ukapita nane limodzi, sizithandiza. 34 Koma ubwerere kumzinda ndipo ukauze Abisalomu kuti, ‘Mfumu, ine ndine mtumiki wanu. Poyamba ndinali mtumiki wa bambo anu koma tsopano ndine mtumiki wanu.’+ Ukakatero, ukatha kunditsutsira malangizo a Ahitofeli.+
-